Africa
From Wikipedia
Africa ndi chigawo chimodzi cha zigawo za pa dziko la pansi ndipo ndi chigawo cha chiwiri kwa madela lomwe kuli anthu ambiri, koma anthu ambiri ali ku Asia. Ku Africa kumakhala 14% ya anthu onse a pa dziko la pansi, chifukwa chiwelengelo cha anthu ku Africaku ndi 900 miliyoni( malinga ndi chiwelengelo cha anthu chomwe chinachitika mu 2005). Gawo la Africa lili ndi mayiko 53, ndipo linazungulilidwa nsi nyanja ya Mediterranean kumpoto, nyanja ya Red Sea kumpoto chakumvuma, nyanja ya Indian kummwera cha kumvuma ndi nyanja ya Atlantic kuzambwe. Pali mayiko 46 a mu Africa ndi 53 kuphatikiza zilumba zonse.
Africa, makamaka kumvuma kwa delari, kumatchuka kwambiri kuti ndi kumene anthu anachokera mtundu wa anthu ndipo anapezako zotsalira za anthu amene analipo zaka 7 miliyoni zapitazo.
Dera la Africa lili mbali zonse ziwiri za mzere wa Equator ndipo nyengo za mudelari zimasiyana siyana kumpoto ndi kummwera kwa mzerewu.
[edit] Kumene kunachokela dzinali
Afri linali dzina la anthu amene ankakhala kumpoto kwa dela la Africa ku malo otchedwa Carthage. –Ca, amatanthauza anthu kapena malo. Anthu ena amaganiza kuti dzina loti Africa linachokela ku: Liu la chilatini lakuti aprica limene limatanthauza malo owala dzuwa kwambiri
Liu la chigiriki aphrike limene limatanthauza malo amene sikumazizira
[edit] Kakhalidwe ka malo ku derali
Dziko lalikulu kwa mbiri kudera la Africa ndi la Sudan ndipo dziko lake laing‘ono kwambiri ndi la Seychelles lomwe ndi chilumba ku mmawa kwa delari. Dziko laling’ono pa gombe ndi Gambia.
Munthu mozama pa nkhani za kakhalidwe ka dziko a Ptolemy (85-165 AD) ndi amene anagawa Africa kuchokela ku dera la Asia ndipo anasiya Nyanja yofiira ngati malire.
[edit] Nyengo, zachilengedwe ndi zomera
Nyengo ku Africa imayambira kukhala yotentha komanso yozizira kwambiri. Kumpoto kwa delari ndi kuchipululu ndi kotentha, pamene pakati ndi kummwera ndi kotentha komanso kuli nkhalango zowilira kwambiri. Pali Madela ena amene kuli nyengo zotentha kwambiri komanso zozizira kwambiri.