Democratic Progressive Movement
From Wikipedia
Democratic Progressive Party (DPP) ndi chipani cha ndale cholamulira mu dziko la Malawi. Chipanichi chinakhazikitsidwa mu Febuluale 2005 ndi msogoleri wa dziko la Malawi, a Bingu wa Muntharika. Iwowa anayamba chipanichi chifukwa chakusagwirizana maganizo ndi chipani cha United Democratic Front (UDF) chomwe iwo anachiyimira pa chisankho. Panali maganizo ndi mphekesera zakuti boma la UDF lomwe linalamulira kuyambira 1994 mpaka 2004 silinachite zokwanira pothetsa mchitidwe wa ziphuphu.
Aphungu ena amene anapambana pa chisankho cha 2004 oyimira zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UDF analowa chipani cha DPP.