Web Analytics Made Easy - Statcounter

See also ebooksgratis.com: no banners, no cookies, totally FREE.

CLASSICISTRANIERI HOME PAGE - YOUTUBE CHANNEL
Privacy Policy Cookie Policy Terms and Conditions
Malawi Congress Party - Wikipedia

Malawi Congress Party

From Wikipedia

Malawi Congress Party (MCP) ndi chipani cha ndale cha ku Malawi. Dzina lake la kale la chipanichi linani Nyasaland African Congress, koma chinasintha kukhala MCP pa nthawi yomwe a Hastings Kamuzu Banda anali mtsogoleri wa dzikoli.

Chipanichi chinapambana pa chisankho mu chaka cha 1961 ndipo chinatenga mipando yonse pa chisankhochi. Kupambana kumeneku kunapangitsa kuti dziko la malawi lipatsidwe ufulu wodzilamulira lokha kuchokera ku boma la chitsamunda. Mu 1966, chipanichi chinapatsidwa mphamvu yokhala chipani chikhacho mu dziko la Malawi. Anthu wonse akulu akulu amayenera kukhala mbali ya chipanichi ndipo amayenera kunyamula ziphaso zosonyeza kuti iwo analidi otsatira chipanichi.

Chipani cha MCP chinatha mphamvu 1993 pamene kunachitika chisankho chomwe anthu ambiri anasankha kuti boma la Malawi likhale la zipani zambiri. Mu 1994, chipanichi chinagonjetsedwa m ndi chipani cha zipani zambiri chomwe chinachitika mu dziko la Malawi.

Ngakhale zinakhala chonchi, chipani cha MCP chinakalibe ndi mphamvu mu dziko la Malawi ndipo chili ndi mphamvu zambiri mu chigawo cha pakati cha dzikoli kumene kuli Achewa ndi Anyanja ambiri.

Pa chisankho chomwe chinachitika mu 2004, mtsogoleri wa chipanichi a John Tembo (amene anali wogwirizana kwambiri ndi a Banda) anapeza 27% ya mavoti onse ndipo chipanichi chinapeza mipando 60 kwa mipando 194 yomwe ya a phungu wa nyumba ya malamulo.

In other languages


aa - ab - af - ak - als - am - an - ang - ar - arc - as - ast - av - ay - az - ba - bar - bat_smg - bcl - be - be_x_old - bg - bh - bi - bm - bn - bo - bpy - br - bs - bug - bxr - ca - cbk_zam - cdo - ce - ceb - ch - cho - chr - chy - co - cr - crh - cs - csb - cu - cv - cy - da - de - diq - dsb - dv - dz - ee - el - eml - en - eo - es - et - eu - ext - fa - ff - fi - fiu_vro - fj - fo - fr - frp - fur - fy - ga - gan - gd - gl - glk - gn - got - gu - gv - ha - hak - haw - he - hi - hif - ho - hr - hsb - ht - hu - hy - hz - ia - id - ie - ig - ii - ik - ilo - io - is - it - iu - ja - jbo - jv - ka - kaa - kab - kg - ki - kj - kk - kl - km - kn - ko - kr - ks - ksh - ku - kv - kw - ky - la - lad - lb - lbe - lg - li - lij - lmo - ln - lo - lt - lv - map_bms - mdf - mg - mh - mi - mk - ml - mn - mo - mr - mt - mus - my - myv - mzn - na - nah - nap - nds - nds_nl - ne - new - ng - nl - nn - no - nov - nrm - nv - ny - oc - om - or - os - pa - pag - pam - pap - pdc - pi - pih - pl - pms - ps - pt - qu - quality - rm - rmy - rn - ro - roa_rup - roa_tara - ru - rw - sa - sah - sc - scn - sco - sd - se - sg - sh - si - simple - sk - sl - sm - sn - so - sr - srn - ss - st - stq - su - sv - sw - szl - ta - te - tet - tg - th - ti - tk - tl - tlh - tn - to - tpi - tr - ts - tt - tum - tw - ty - udm - ug - uk - ur - uz - ve - vec - vi - vls - vo - wa - war - wo - wuu - xal - xh - yi - yo - za - zea - zh - zh_classical - zh_min_nan - zh_yue - zu -