Web Analytics Made Easy - Statcounter

See also ebooksgratis.com: no banners, no cookies, totally FREE.

CLASSICISTRANIERI HOME PAGE - YOUTUBE CHANNEL
Privacy Policy Cookie Policy Terms and Conditions
Bakili Muluzi - Wikipedia

Bakili Muluzi

From Wikipedia

A Elesoni Bakili Muluzi, amene anabadwa pa 17 Malichi 1943 anali mtsogoleri wa dziko la Malawi kuyambira 1994 mpaka 2004.

[edit] Moyo wawo wakale

A Muluzi anabadwira mmboma la Mangochi ndipo anagwirako ntchito mmboma. A Muluzi anakhala mmaudindo wosiyana siyana mu chipani cha Malawi Congress Party chomwe chinkalamulira dzikoli.

[edit] Utsogoleri wa dziko la Malawi

A Muluzi, amene ankayimira chipani cha United Democratic Front (UDF) anakhala mtsogoleri wa dzikoli pamene anapambana pa chisankho cha utsogoleri cha zipani zambiri pomwe iwo anapambana ndi 47%. Iwowa anapeza ma voti ambiri kuposa mtsogoleri wa kale amene analamulira dzikoli kuyambira 1964, a Hastings Kamuzu Banda. A Muluzi anapambanso pa chisankho chomwe chinachitika mu 1999 popeza 52% ya mavoti onse, kuwaposa a Gwanda Chakuamba amene ankawoneka ngati apambana pa chisankhocho. Mu 2002, anthu owathandizira ankafuna kusintha malamulo akuti mtsogoleri aziyima pa chisankho kawiri kokha ndi cholinga chakuti a Muluzi ayime kachitatu. Maganizo amenewa anasiyidwa pamene anthu ena anatsutsana nalo ganizoli pochita ziwonetsero. Iwo anasiya boma mu mwezi wa Meyi 2004, ndipo amene anapambana chisankho anali a Bingu wa Muntharika amene ankayimiranso chipani cha UDF.


A Muluzi anali ndi maudindo muboma la a Hastings Kamuzu Banda koma iwo anali mmodzi mwa amene ankatsutsana ndi boma la chipani chimodzi. Ngakhale zinali chonchi, utsogoleri wa a Banda unali ndi nkhani zina zosakhala bwino, mwachitsanzo pamene iwo anagulitsa chimanga chomwe dzikoli linkasunga pa nthawi yomwe kunali njala komanso posokoneza ndalama zomwe zinapezeka pa malonda ndi maiko ena a chimangacho, ngakhale maiko ena akunja ankayesayesa kuti afufuze chomwe chinachitika. Anthu ambiri amaganiza kuti ndalamazi anagawana a Muluzi ndi wotsatira awo ndipo zinasungidwa ku nyumba zosungirako ndalama za maiko a kunja. Ngakhale kunali nkhani zambiri zotele, a Muluzi anali mtsogoleri wotchuka mu dzikolu makamaka ku madera a ku mmwela kwa dzikoli.

[edit] Moyo wawo atasiya utsogoleri

Iwo anapitiliza kukhala mtsogoleri wa UDF ngakhale anasemphana maganizo ndi amene iwo anamusankha kukhala mtsogoleri, a Bingu wa Muntharika. A Muntharika anasiya chipani cha UDF ndikukapanga chipani chawo cha Democractic Progressive Party (DPP).


A Muluzi anamangidwa pa 27 Julaye 2006 pa milandu yokhudza ziphuphu koma anamasulidwa tsiku lomwelo. Patangopita ma ola ochepa, munthu amene ankafufuza za mulandu wa a Muluzi, a Gustav Kaliwo anaimitsidwa pa ntchito ndi a Muntharika. Pa chifukwa chimenechi, amene amazenga mulandu wa a Muluzi, a Ishmael Wadi anaimitsa mulanduwu.


Kuyambira mwezi wa Malichi 2007 anthu ena anayamba kunena kuti a Muluzi adzaimenso pa chisankho chomwe chidzachitike mu 2009 ndipo anawapatsa nthawi yakuti anene ngati ankafuna kudzaima pa chisankhocho. Pa 11 Malichi, a Muluzi analengeza kuti adzaimadi, ndipo otsatira awo ena ngati a Brown Mpinganjira komanso a Sam Mpasu, amene koyambilira ankafuna kudzaimira UDF pa chisankhochi, analengeza kuti sadzaima chifukwa cha chidwi chomwe a Muluzi anawonetsa kudzaima.


Ngakhale zili chonchi, pali kusamvetsetsa pa zomwe malamulo a dzikoli amanena zokhudza kuima pa chisankho cha atsogoleri akale chifukwa malamulowo amanena kuto mtsogoleri sangaime kachitatu kotsatizana ndipo a Muluzi akufuna kuima chifukwa sanaime pa chisankho chomwe chinachitika 2004. Pa chifukwa chimenechi, anthu ambiri akufuna kuti malamulowo asinthidwe ndipo kuti mawu onena zotsatizana achotsedwe mu malamulowo.


aa - ab - af - ak - als - am - an - ang - ar - arc - as - ast - av - ay - az - ba - bar - bat_smg - bcl - be - be_x_old - bg - bh - bi - bm - bn - bo - bpy - br - bs - bug - bxr - ca - cbk_zam - cdo - ce - ceb - ch - cho - chr - chy - co - cr - crh - cs - csb - cu - cv - cy - da - de - diq - dsb - dv - dz - ee - el - eml - en - eo - es - et - eu - ext - fa - ff - fi - fiu_vro - fj - fo - fr - frp - fur - fy - ga - gan - gd - gl - glk - gn - got - gu - gv - ha - hak - haw - he - hi - hif - ho - hr - hsb - ht - hu - hy - hz - ia - id - ie - ig - ii - ik - ilo - io - is - it - iu - ja - jbo - jv - ka - kaa - kab - kg - ki - kj - kk - kl - km - kn - ko - kr - ks - ksh - ku - kv - kw - ky - la - lad - lb - lbe - lg - li - lij - lmo - ln - lo - lt - lv - map_bms - mdf - mg - mh - mi - mk - ml - mn - mo - mr - mt - mus - my - myv - mzn - na - nah - nap - nds - nds_nl - ne - new - ng - nl - nn - no - nov - nrm - nv - ny - oc - om - or - os - pa - pag - pam - pap - pdc - pi - pih - pl - pms - ps - pt - qu - quality - rm - rmy - rn - ro - roa_rup - roa_tara - ru - rw - sa - sah - sc - scn - sco - sd - se - sg - sh - si - simple - sk - sl - sm - sn - so - sr - srn - ss - st - stq - su - sv - sw - szl - ta - te - tet - tg - th - ti - tk - tl - tlh - tn - to - tpi - tr - ts - tt - tum - tw - ty - udm - ug - uk - ur - uz - ve - vec - vi - vls - vo - wa - war - wo - wuu - xal - xh - yi - yo - za - zea - zh - zh_classical - zh_min_nan - zh_yue - zu -